Nkhani

Ndimamufuna kwambiri

Anatchereza

M’mudzi mwathu mudabwera mtsikana wina wake yemwe ndidakondweretsedwa naye. Ndidachita machawi kumufunsila ndi kumuuza kuti ndimamukonda koma sadandiyankhe.

Mwa chifuniro chake adavomera mbalame zocheredwa. Inde, mwamuna wina.

Miyezi iwiri yadutsa koma ine ndidakamulotabe mkazi ameneyu. Sindikusamala kuti ali ndi mwamuna wina.

Panopa ndikamuyankhula amati tizingocheza basi. Ndikamukhumudwira amabwera ndi kumandipepesa.

Mtsikanayu ndamukondetsetsa ndipo ndikufunisitsa titakhala pa chikondi osati zomwe iye akufunazo. Nditani ine Azakhali kuti ndimuwine mtsikana ameneyu.

ZM

Dedza

Achimwene!!!!! Chikondi sakakamiza. Inu zoona mwamukonda mkazi ameneyo koma ngati iye sadakukondeni sizingatheke kumukakamiza.

Chikondi chimayenera kukhala cha mbali zonse. Musaiwale kuti ali yense ali ndi zokonda zake. N’kutheka kuti inu mulibe zomwe iye amakonda mwa mwamuna.

Musiyeni ameneyo. Musataye naye nthawi yanu. Athanso kukubweretserani mavuto. Ngati adavomera mwamuna wina ndiye kuti inu sakukukondani.

Ngati mumamupatsa ndalama dziwani kuti akungokudyerani basi.

N’kutheka kuti akuganiza kuti mungofuna kumutayitsa nthawi. Inu pezani mkazi wina woti akukondeni. Akazi woti mukuchita kuwakakamira pena pake amadzakuzunza n’kumati kuti pajatu unkandikakamiza kuti ndikukonde. Ndiye zimenezo zimawawa kwambiri.

Akazi alipo ambiri ndipo nawonso akufuna amuna achikondi.

Anatchereza.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Check Also
Close
Back to top button