Sensasi ili mkati

Pamene kalembera wa anthu ndi nyumba ali mkati, mafumu ena ati akuyembekezera kuti mavuto amene amakumana nawo achepa chifukwa boma limagwiritsa ntchito zotsatira za kalemberayo popereka zofunika kwa Amalawi.

Kalemberayo, amene amachitika pakatha zaka 10 zilizonse, adayamba pa 3 mwezi uno ndipo akuyembekezeka kudzatha pa 23.

Wogwira ntchito ya kalembera kulembera banja lina ku Lilongwe

Polankhula ndi Tamvani, T/A Mlauli ya ku Mwanza, T/A Chindi ku Mzimba komanso T/A Mkanda ku Mchinji adanena payekhapayekha kuti ali ndi chiyembekezo kuti mavuto amene adza kaamba ka kukula kwa chiwerengero achepa.

“Vuto lalikulu limene tili nalo ndi la madzi. Ngakhale anthu akumanga nyumba zofolera ndi malate, madzi tikumwabe m’zitsime zosasaamalika. Izi zimadzetsa matenda amene timakavutikanso nawo kuchipatala,” adatero Mkanda.

T/A Chindi adati ngakhale kuli mavuto ena monga kusowa vuto la zaumoyo, nkhani yamadzi siyimugoneka tulo.

“Amayi amadzuka mbandakucha kukatunga madzi dzuwa litakwera. Kungochedwa pang’ono ndiye kuti pakhomo pawo. Mukhonza kuona ngati madzi akukanganiranawo ndi a pampope, koma ayi ndi a pachitsime,” adatero Chindi.

T/A Mlauli wa ku Neno idati vuto la madzi likusautsa, makamaka m’chilimwe pomwe dzuwa likuomba kwambiri. Iye adati izi zikukhudzaa kwambiri dera lake limene ndi lotentha kwambiri.

“Akukonza zina ndi zina, koma pa nkhani ya madzi, tisanamizanepo zinthu zikuyipirayipira. Mijigo ili apo ndi apo koma chiwerengero cha anthu ofuna madzi abwino chikungokwererabe,” adatero Mlauli.

Kalemberayu akuyamba kumene, padali mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo la kuchedwa kwa malipiro a ogwira ntchitoyi 25 000 pomwe adangolandira K20 000 mmalo mwa K120 000 imene amayenera kulandira ataphunzira ntchitoyi. Ogwira ntchito enanso adandaula kuti sanapeze nawo lamya zogwirira ntchitoyo. Vuto lina lidali la kubedwa kwa zipangizo za ogwira ntchitoyi ku Ntcheu.

Mneneri wa nthambi yoona za kalemberayu ya National Statistical Office (NSO) Kingsley Manda adatsimikiza za mavutowa koma adati zonse zili tayale tsopano.

“Chilichose chilibwino, onse adalandira ndalama zawo, tawatsimikizira kuti mayunitsi afika sabata ino koma awo amafuna lamyawo, tawafotokozera kuti lamya nzawokhawo omwe akuyenda m’midzi kutenga mafigala,” adatero Manda.

Iye adati vuto lalikulu lomwe lidalipo lidali lokhudza netiweki yotumizira ma figala makamaka mmadera momwe mulibe netiweki koma vutolonso adalikonza.

“Padali vuto la netiweki m’madera ena ndiye poti makina omwe tikugwiritsa ntchito ngolira netiweki kuti tilumikizane, tidapereka galimoto zomwe akumagwiritsa ntchito kuyenda kukafika pomwe pali netiweki n’kutumiza,” adatero Manda.

Mmodzi mwa owelengera anthuwa ku Mpsupsu m’boma la Zomba amene sanadzitchule dzina adati pa tsiku akumawerenga makomo osachepera 40.

Iye adati ngakhale nyumba za derali zili patalipatali koma akumakwanitsa kuwerenga anthu ochuluka chotere chifukwa kufunsa mafunso pogwiritsa ntchito tablet sizikumatenga nthawi kuti atsirize.

M’modzi wa anthu amene awerengedwa kwa Jali m’boma la Zomba Lones Kamwana adati mphindi zosaposera 45 zimene adafunsidwa mafunso akuti mphindizi zidali zopindulitsa kwa iye mwini ngakhalenso ku dziko.

“Mafunso ake akumufukula munthu kuchokera pa phata zinthu zimene a Malawi tikayankha mwachilungamo zithandizira kuti dziko lathu lino likhale lotukuka,” adatero Kamwana.

Kalembera wa m’chaka cha 2008 chiwerengero cha anthu chidapezeka kuti ndi 13 077 160. Lipoti la kalemberayu limasonyeza kuti anthu 48 mwa anthu 100 aliwonse amamwa madzi a pamjigo, anthu 18 pa 100 aliwonse amamwa m’zitsime zosatetezedwa.

Lipotili likusonyezaso kuti anthu 43 pa 100 amakhala mnyumba zawedewede, anthu 34 pa 100 amakhala mnyumba zowonekako bwino ndipo 23 pa 100 aliwose amakhala m’nyumba zolongosoka.

Malinga ndi NSO, chiwerengero cha Amalawi chikhonza kufika pa 17 931 637 chaka chino.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.

Powered by