Nkhani

Sitilemba akunja—Ansah

Listen to this article

Pamene kalembera wachisankho walowa gawo lachisanu, mkulu wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah wati Amalawi asade nkhawa, chifukwa anthu a kunja salembetsa nawo m’kaundula.

Ansah adanena izi potsatira ndemanga za ena kuti pali chiopsezo choti nzika zina za dziko la Mozambique zikhonza kulembetsa m’kaundula m’boma la Mulanje. Malinga ndi anthu ena, pali chiopsezo kuti anthu ena a ku Mozambique akhonza kufuna kulembetsa nawo, makamaka ku Limbuli ndi Muloza, komwe ndi dera la m’malire ndi Mozambique.

Koma Ansah adanenetsa: “Taika ndondomeko zonse kuti pasakhale wakunja woti walembetsa. Izi tikuchita poonetsetsa kuti pali mamonitala a kuderalo amenenso adzaonetsetse kuti ofuna kulembetsa ali ndi chitupa cha unzika.”

Mkulu wa nthambi yoona za kalembera wa unzika m’boma la Mulanje, Wellingtone Kalambo wati akumanapo ndi nzika za ku Mozambique zofuna kulembetsa nawo mavoti.

“Taonapo mafumu a ku Muloza akupereka umboni kuti munthu ndi m’Malawi, koma kuwafunsitsa, tidapeza kuti ndi a ku Mozambique,” adatero Kalambo.

Kalembera wa chisankho adalowa m’gawo lachisanu Lolemba ndipo likuyembekezeka kudzatha pa … Malinga ndi MEC, anthu 3 271 744 adalembetsa m’magawo apitawa, pomwe MEC imayembekezera kulembetsa anthu 4 619 174. Izi zikusonyeza kuti anthu 81 mwa 100 alionse amene amayenera kulembetsa ndiwo adatero.

Kutsika kwa anthu amene akulembetsa kwakhudza akadaulo, a mabungwe ndi zipani zandale zina.

Katswiri wa zandale wa ku Chancellor College Ernest Thindwa wati

mchitidwe wamphwayi kukalembetsa ukhonza kukhala kukhumudwa kwa Amalawi

ndi mchitidwe wa andale omwe amasintha mawanga akasankhidwa m’maudindo.

“Mwina anthu adagwa mphwayi ndi nkhani za zisankho

chifukwa amakhumudwa ndi mchitidwe wa atsogoleri omwe amalonjeza

zinthu zina nthawi ya kampeni koma osazikwaniritsa akasankhidwa,” adatero

Thindwa.

Koma zipani zandale, zaalunjika ponena kuti bungwe la MEC silinafalitse bwino uthenga wa kalembera chifukwa likulimbikira pofalitsa mauthenga pa wailesi ndi nyuzipepala basi, mmalo mopitanso kumaderawo.

Mneneri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga, wati kafukufuku wawo adaonetsa kuti bungwe la MEC silidafalitse uthenga mokwanira m’madera.

“Tikawafunsa bwanji sanalembetse, anthu m’madera amati samadziwa zoti kalembera wafika m’dera lawo. Ngati chipani, tikumapita m’maderamu kumema anthu,” adatero Ndanga.

Mlembi wamkulu wag ulu la United Transformation Movement (UTM) Patricia Kaliati komanso mlembi wamkulu wa Malawi Congress Party (MCP) Eissenhower Mkaka adagwirizana ndi Ndanga podzudzula MEC.

“Ndikunena pano ndili ku Mulanje kumene kalembera ali mkati koma sindinaone galimoto ya MEc ngakhale chimkuzamawu kumema anthu kukalembetsa.

Mkaka adati chipani chawo, chomwe chakhala chikupempha MEC kuti ibwereze kalembera m’madera ena, chimayembekezera kuti pofika gawo lachinayi la kalembera, zinthu zikhala zitasintha koma mmalo mwake zikunkira kuonongeka.

“M’gawo loyamba ndi lachiwiri, zidali zomveka kuti uthenga udali usadamwazidwe mokwanira koma m’gawo lachinayi tizikamba nkhani imeneyi? Ayi sizoona MEC ikadawonapo bwino,” adatero Mkaka.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adagwirizana ndi zipanizi kuti MEC yalephera kumwaza mauthenga a kalembera.

“Ndidali ku Thyolo ndi Luchenza komwe anthu samaonetsa chidwi ndipo n’tafunsa, makhansala ngakhaleso anthu amati sadalandire uthenga uliwonse woti kukuchitika kalembera m’dera lawo kutanthauza kuti ntchito ikadalipo,” adatero Duwa.

Koma malinga ndi Ansah, palibe kuwiringula kulikonse koti mauthenga sadamwazidwe chifukwa MEC ndi mabungwe ena monga National Initiative for Civic Education (Nice) Trust ayesetsa kumwaza mauthenga.

“Kupatula njira yomwaza mauthenga pa wailesi, timagwiritsanso ntchito galimoto zokhala ndi zimkuzamawu. M’gawo loyamba, tidagwiritsa ntchito galimoto 15, gawo lachiwiri galimoto 14, gawo lachitatu galimoto 18 ndipo gawo lachinayi galimoto 17,” adatero Ansah.

Iye adati bungweli lidzaunika pamapeto pa zonse ngati n’koyenera kubwereza ntchito ya kalembera m’maboma omwe sizidayende bwino.

Kalembera wa zisankho wachitika kale m’maboma a Kasungu, Salima, Dowa, Ntchisi, Dedza, Nkhotakota, Lilongwe, Chikwawa, Ntcheu, Blantyre ndi Mwanza.—zoonjezera: madalitso kateta, mtolankhani wa mec

Related Articles

Back to top button
Translate »