Nkhani

Woyendetsa ambulansi ataledzera amangidwa

Dalaivala wa ambulansi ya pachipatala cha boma cha Chiradzulu zake zada atagwetsa galimotoyo m’ngalande chifukwa choledzera.

Malinga ndi kanema imene yakhala ikuzungulira m’masamba a mchezo, dalaivalayo akuoneka ali thapsa ndi mowa, akukanika kulankhula zomveka komanso kuima bwinobwino.

Ali ku Chichiri: Thumba

Padakalipano mkuluyo ali pa alimande kundende ya Chichiri ndipo akaonekera kubwalo la milandu Lolemba.

Pakanemapo mkuluyo adachita anthu ena adachita kumugwira uku ndi uko. Anthuwo sadamusiye ngakhale amachita makani n’kumakana kuti asamujambule, apatu nkuti galimotoyo italowa m’ngalande mbali mwa msewu wochokera ku Njuli kupita ku Chiradzulu.

Galimotolo ndi gulu la galimoto zatsopano zomwe boma lapereka m’zipatala. Koma mwatsoka, m’galimotomo adanyamulamo wodwala amene amapita naye pachipatalapo.

Andrew Thumba wa zaka 37, yemwe amayendetsa MG 566 AM adathera m’manja mwa anthu omwe adamugwira ndi kuiperanso nkhaniyo kwa akuluakulu a boma.

Ndipo mneneri wa polisi m’bomali Yohane Tasowana watsimikiza za nkhaniyi.

Iye adati mkuluyu akuyankha mlandu woyendetsa galimoto ataledzera mosemphana ndi gawo 128 la malamulo oona za pamsewu m’dziko muno.

Tasowana adatsimikizanso kuti m’galimotomo mudali wodwala yemwe adangonyamulidwa pa njinga ndi anthu achifundo kuthamangira naye kuchipatalako.

Koma mkulu woona za umoyo m’boma la pankhaniyo ati chifukwa ili ku khoti.Chiradzulu Jameson Chausa adakanitsitsa kulankhulapo

“Nkhaniyi ilowanso ku bwalo la milandu Lolemba, ndipo dalaivalayu akadali m’manja mwa apolisi,” adalongosola Chausa.

Thumba, amachokera m’mudzi mwa Truwa, T/A Kadewere, m’bomalo.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adati zomwe adachita dalaivalayo zidali zosayenera komanso sakuyenera kupitiliza kugwira ntchito m’chipatala koma apite ku malo ena.

Iye adati ntchito yoyendetsa galimoto yonyamula odwala njofunika munthu wokhwima m’maganizo komanso wolemekeza odwala, choncho pakapezeka dalaivala wa khalidwe loipa, azimuchotsa msanga kuti asamaononge mbiri ya anzake.

“Pali woyendetsa galimoto zonyamula odwala ambiri omwe ali akhalidwe komanso mitima yabwino, takhala tikuwaona akuika miyoyo yawo pachiswe populumutsa odwala; mbiri ya awawa imaonongeka nawo chifukwa cha ochepa omwe alibe khalidwe,” adalongosola Jobe.

Iye adatinso zipatala zizikonza maphunziro a oyendetsa galimotozo pafupipafupi owaphunzitsa zina mwa ngodya za ntchito zawo.

Jobe adati bungwe lake limalandira madandaulo ochokera kwa anthu kudandaula ena mwa madalaivala a galimotozo monga dalaivala wina m’boma la Ntcheu, yemwe adasiya maliro panjira patatsala mtunda wapafupifupi makilomita atatu ndi komwe amakatulako ati chifukwa cha mafuta.

Iye adatsindika kuti madalaivala omwe akuona kuti sangakwanitse m’zipatala aziwasuntha n’kukawaika m’malo ena omwe angakwanitse.

“Koma tikupempha nkhani ngati izi kuti zisamafooketse madaivala omwe akugwira ntchito zawo bwino ndi mwachikondi,” adalongosola iye.

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.