‘Zipani zisaope achinyamata’

Bungwe lolimbikitsa achinyamata pa ndale mu Africa la Centre for Young Leaders in Africa (CYLA), lapempha zipani zandale m’dziko muno kuti zisaope kugwira ntchito ndi achinyamata.

Malingana ndi mtsogoleri wa pulogalamu yotchedwa Programme for Young Politicians in Africa (PYPA) ku bungwe la CYLA wochokera m’dziko la Zambia, Anna Mate, achinyamata asakhale chiopsezo koma chitetezo pa ndale za m’chipani.

Mate: Achinyamata ndi ambiri

Mate wati zipani zambiri zimene bungwe la CYLA lagwira nazo ntchito zimaonetsa kuti zikupereka mfundo zokhwima ndi cholinga choti achinyamata azichita mantha n’kubwerera mmbuyo pa ndale.

“Ife monga olimbikitsa achinyamata pa ndale tidakumana ndi akuluakulu a zipani zandale zokhazikika m’dziko muno ndipo tawalimbikitsa kuti agwire limodzi ntchito ndi achinyamata pa ndale,” adatero Mate.

Iye adati ali ndi chikhulupiliro kuti uthengawu wadza m’nthawi yake potengera kuti nzika za dziko lino zikukonzekera kukaponya voti ya patatu chaka cha maya.

Iye adatinso zipani zomwe zatsogoza achinyamata m’maudindo zimakhala ndi mwayi waukulu wopititsa patsogolo kuchuluka kwa owatsatira potengera kuti achinyamata ndi omwe akutenga gawo lalikulu la chiwerengero cha dziko lino.

Iwo apemphanso achinyamata kuthandizana komanso kulimbikitsana pamene akufuna kutengapo gawo pa ndale.

Pakadali pano CYLA ikupitirira kufikira achinyamata ndi cholinga chowadzindikiritsa za udindo wawo pa ndale za dziko lino kuphatikizapo kuwalimbikitsa kukaponya voti pa zisankho za patatu za chaka cha mawa.

Pothirirapo ndemanga yemwe akufuna kudzaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP), ku Salima Gerald Phiri adati zipani zayamba kuthandiza oyimira posatengera zaka za munthu.

“Atsogoleri asamangotigwiritsa ntchito achinyamata poyambitsa zipolowe basi. Nthawi yakwana yoti tigwire ntchito limodzi ndi akuluakulu popanda kuopsezedwa,” adatero Phiri.

Share This Post

One Comment - Write a Comment

Comments are closed.