Nkhani

Zisangalalo zafika, samalani

Listen to this article

Yafika nyengo ya zisangalalo za Khrisimasi ndi Nyuwere ndipo ena ayamba kale mapwando pomwe ena akukonzekera masangalalidwe osiyanasiyana monga kupita ku madansi, kudzathibula mowa ndi kuyenda maulendo osiyanasiyana.

Koma izi zili apo, unduna wa zaumoyo wachenjeza kuti chiopsezo cha mlili wa Covid-19 n’chachikulunso m’nyengoyi potengera kuti ndi nyengo yakusakanikira kwa mphepo ndi chifunga zomwe ndi abwenzi a Covid-19.

Malango: Covid-19 ikadalipo

Mneneri waundunawu Joshua Malango wati kupatula mphepo ndi chifunga, mliliwu ukadali waukulu m’maiko ena kutanthauza kuti kufika kwathu kuno n’kufala mwachangu n’kosavuta makamaka panyengoyi.

“Chodandaulitsa kwambiri nchoti anthu tatayirira za njira zodzitetezera, masiku ano zikuoneka kuti munthu ovala masiki ndiye akuoneka wachilendo ngati otsalira komanso zosamba m’manja tidaiwalako,” watero Malango.

Iye wati anthu akuyenera kukondwera koma pokonzekera zikondwerero zawo zosiyanasiyana asaiwale kuikapo njira zodzitetezera kuti nyengoyi ikamatha, tonse titulukemo bwinobwino popanda kutenga Covid-19 ndi matenda ena.

“Mwachitsanzo, ngati mukukonzekera phwando, dansi kapena masewero a mtundu uliwonse komwe mukuyembekezera khamu la anthu, onetsetsani kuti mwayikapo ndondomeko yoti obwera adzakhale ndi masiki, pakhale madzi osamba m’manja komanso khalani motalikana,” watero Malango.

Mkati mwa sabatayi, akadaulo adachenjeza kuti Covid-19 itabukanso mwa moto m’dziko muno, kukhoza kukhala kovuta kuthana nayo.

Kadaulo pa zamaphunziro Benedicto kondowe naye wati posangalala m’njira zosiyanasiyana, makolo asayiwale kuti teremu yoyamba ya sukulu idzatsegulidwa pa 4 January 2021 ndipo ndondomeko yoti ana popita kusukulu adzakonzeke motani siyidatuluke.

Iye wati zimakhala zomvetsa chisoni komanso zochedwetsa mwana kuti pomwe sukulu zatsegulidwa iye akadali pakhomo kudikira makolo alandire malipiro a January chifukwa uku anzake amakhala akuphunzira.

“Muganizire makamaka mwana yemwe akukayamba Folomu 1, mmalo moti apite limodzi ndi anzake azikazolowera limodzi, iye ali kunyumba mpaka mwezi watunthu. Apa amafa kawiri chifukwa pa mwezi umenewo anzake ayimitsa kale maziko a m’maphunziro osiyanasiyana iye watsala mmbuyo komanso akamabwera zimamusokoneza chifukwa amakhala ngati mlendo sukulu yonseyo ndi iyeyo basi,” watero Kondowe.

Kadaulo pa zachuma Loryn Nyasulu wati ndalama iliyonse yomwe kholo limapeza likhoza kupanga nazo zooneka malingana ndi momwe khololo lapangira bajeti ya ndalamazo.

Iye wati m’nyengo ngati iyi, chomwe chimafunika kwambiri n’kukhala pansi kulingalira za zinthu zofunika kwambiri ndalama zake n’kuika padera kenako zotsalazo n’kuzipangiranso bajeti ina ya zinthu zomwe n’zofunika pakhomopo koma zinthu sizingasokonekere zinthuzo zitapanda kuchitika.

“Kugwiritsa ntchito ndalama mwaphindu zimatengera momwe munthu wayipangira bajeti ndalamayo. Kuona kuti kodi momwe ndilili panopa, zofunika kwambiri kwa ineyo nziti ndipo zikufunika ndalama zingati n’kuyikiratu pambali ndalamazo,” watero Nyasulu.

Apolisi nawo ati anthu asayiwale kuti chaka chilichonse iyi ndiyo nyengo yomwe kumachitika umbanda komanso ngozi za pamsewu zambiri chifukwa cha kusasamala kwa anthu posangalala.

Wachiwiri kwa mneneri wapolisi m’dziko muno Peter Kalaya wati apolisi akhala ali ponseponse oyenda pansi, a m’galimoto komanso odziwa za m’madzi kuonetsetsa kuti paliponse pali chitetezo chokwanira.

“Timanena chaka ndi chaka kuti pochoka pakhomo osachokapo nonse, ngati aliyense akufuna kukasangalala, mukhoza kugawana kuti ena apite pa Khrisimasi kenako pa nyuwere adzapite enawo koma nthawi zonse pakhomo pazikhala munthu wanzeru zake.

“Chinanso anthu ali ndi khalidwe lokonda kulengeza komwe ali ndi zomwe akuchita pa Intaneti. Izi zimathandiza kupereka uthenga kwa mbava za makomo omwe mulibe chitetezo chifukwa amadziwa kuti khomo lakuti eni ake kulibe ali ku nyanja,” watero Kalaya.

Iye watinso onse oyendetsa magalimoto adziwiretu kuti apolisi a pamsewu akhala ali paliponse mmisewu ndipo sasekelera galimoto iliyonse yosayenera kuyenda pamsewu komanso madalayivala onse ophwanya dala malamulo.

“Ngozi zambiri zimachitika chifukwa chothamanga mosakhala bwino, galimoto zosayenera kuyenda pamsewu komanso kuyendetsa munthu ataledzera ati chifukwa akusangalala koma mapeto ake amaononga nazo miyoyo ya anzawo komanso yawo,” watero Kalaya.

Panyengo ngati yomweyi chaka chatha cha 2019, ngozi 14 zidachitika ndipo anthu 8 adamwalira pakati pa 24 ndi 26 December pomwe ngozi 48 zidachitika pa 1 January 2020 pokha ndipo anthu atatu adamwalira pomwe 26 adavulala.

Related Articles

Back to top button