Nkhani

Angwanjula osalembetsa

Ngati mukuyesera kuimba foni koma sizikutheka, kapena mayunitsi sakulowa, ingodziwani kuti nambala yanu sidalembetsedwe ndipo ayithothola.

Izi ndi zomwe anthu ena maka amene amagwiritsira ntchito netiweki ya TNM akumana nazo kucha kwa pa 1 October. Pamene ogwiritsira ntchito Airtel adaonanso mbonaona Lachitatu.

Anthu akulembetsa manambala awo a foni

Izi zikutsatira ganizo la boma lodzera ku bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra) kuti kampani za foni zam’manja zilembetsedwe.

Kulembetsako kumatha mpaka pa 30 September 2018 ndipo aliyense amene sadalembetse amamudulira kuti asathenso kulandira, kuimba foni yake komanso uthenga wa pafoni sumatheka.

Malinga ndi mkulu woona zamalonda ku kampani ya TNM, Daniel Makata, pofika pa 30 September n’kuti kampani yake itadula nambala 25 pa 100 paliponse.

“Kutanthauza kuti makasitomala 75 pa 100 alionse alembetsa ndipo nambala zawo sizinadulidwe,” adatero Makata.

Pamene wolankhulira kampani ya Airtel Nora Chavula adati kampani yake idalandira anthu ambiri kumapeto kwa masiku otsekera ndiye pofika Lachiwiri sabata ino n’kuti asadamalize kulowetsa anthu onse.

Komabe Chavula adati anthu amene sadalembetse awachotsa pa netiweki yawo malinga ndi lamulo lomwe adalandira ku boma.

Kwa anthu amene nambala zawo zadulidwa atha kupita kukalembetsa ndipo nambala yawo idzayambiranso kugwira ntchito pasadathe maola awiri.

“Ndipo anthu adziwe kuti sakupemphedwa kulipira kanthu pamene akukalembetsa. Ngati m’foni mwawo mudali mayunitsi pamene timadula nambala yawo, akakalembetsa mayunitsiwo adzawapeza,” adatero Makata.

Iye adati kampani yawo idalemba anthu oposera 2 500 m’madera onse kuti alembe onse amene ali pa netiweki ya TNM.

Related Articles

Back to top button