Anthu alembetsa mwaunyinji—MEC
Bungwe loyendetsa zisankho la MEC lati anthu chiwerengero cha anthu omwe alembetsa kuti adzavote pa Chisankho Chachikulu cha pa 16 September 2025 chili pa 7 200 905, poyerekeza ndi 10 957 490 amene adzakhale atakwana zaka 18 pa tsikulo.
Izi zikusonyeza kuti anthu 66 mwa 100 amene amayenera kulembetsa atero.

Malingana ndi kalatayo, mwa anthu olembetsawo, 3 087 563 ndi abambo kusonyeza kuti mwa anthu 100 alionse amene alembetsa 43 ndi abambo. Amayi amene alembetsa alipo 4 113 342, kusonyeza kuti mwa anthu 100 alionse amene angadzavote, 57 ndi amayi.
M’chaka cha 2019, pomwe Amalawi adavota pa chisankho chapita, anthu 6.8 miliyoni ondi omwe adalembetsa.
Izi zili apo, chiwerengero cha anthu omwe alembetsa pa kalembera wachibwereza ndi wotsika kwambiri.
“Monga mukudziwa, tidakhazikitsa ckalembera wachibwereza potsatira chigamulo cha bwalo la milandu, kalembera ameneyo tinkayembekezera kuti anthu 271 854 alembetsa koma anthu 24 708 ndiwo adalembetsa,” yatero kalatayo.
Zipani za DPP, Aford ndi UTM zati ngakhale bungwe la MEC lidapangitsa kalembera wobwerezayo, palibe chomwe chidathandiza chifukwa mavuto aakulu omwe adachititsa chibwerezacho sadakonzeke.
Mneneri wa UTM a Felix Njawala ati zipani za ndale ndi gawo limodzi lalikulu kwambiri pa chisankho ngati chomwe chikubwerachi koma zodandaulitsa n’zoti MEC siimagwiritsa ntchito maganizo onse omwe zipanizo zimapereka.
“Takhala tikunena za mavuto omwe adalipo pa kalembera wa chisankhochi koma palibe n’chimodzi chomwe chimene MEC idagwiritsa ntchito. Mwachitsanzo, tidanena za kuchepa kwa masiku achibwereza pano ndi izi tikumva kuti anthu ambiri sadakalembetsenso pa chibwereza,” adatero a Njawala.
Iwo adati kalembera wachibwereza ali mkati, iwo adapita kwawo kukaona momwe zikuyendera koma adakhumudwa kupeza kuti mmalo ena olembetsera anthu adali asadayambe kufika kaamba koti uthenga sudawapeze nthawi yabwino.
“Madera a m’tauni ndi a kumudzi n’zosiyana kwabiri chifukwa m’tauni uthenga siuchedwa chifukwa muli njira zambiri zofalitsira uthengawo koma kumidzi n’kovuta chifukwa anthu amadalira kuti atsimikize kaye mphekesera,” adatero a Njawala.
Kalembera wachibwereza adachitika kaamba koti nthawi yomwe kalembera woyamba ankayamba, nthambi yochita kaundula wa unzika la NRB lidali lisadamalize kupeleka zaunzika kwa anthu oyenera kuponya voti.
Kusamvana koyamba kudalipo kalemberayo asadayambe bungwe la MEC litatsegulira ndondomeko yachisankho nkulengeza kuti igwiritsa ntchito zitupa za unzika polemba anthu m’kaundula wa chisankho.
Mneneri wachipani cha DPP a Shadrick Namalomba adati chipani chawo sichidagwirizane ndi ganizolo chifukwa m’madera ambiri anthu omwe adafika zaka 18 ndipo ndi oyenera kuponya voti adalibe zitupa za unzika.
“Kalembera wa unzika ali ndi mavuto ambiri zedi monga makina kuonongeka, zitupa kuchedwa kutuluka komanso zipangizo monga mapepala olembetsera mmalo ena samapezeka mokwanira ndiye kuli bwino agwiritse ntchito umboni wina osati za unzika zokha ayi,” adatero a Namalomba.
Pa nkhani ya kalembeera wachibwereza, iwo ati DPP siyikukhutirabe ndi chibwerezacho kaamba koti nthawi idali yochepa komanso chipanicho chikuona ngati anthu ena aponderedzedwa kaamba ka malire omwe MEC idapereka kwa olembetsa pachibwereza.
Mneneri wa Aford a Annie Maluwa adati mavuto ngati opangitsa chibweretsa sakadakhalapo bungwe la MEC likadamva pempho loti pakhale zizindikiro zingapo zolembetsera m’kaundula wa chisankho.
“Akadalingalira zoikapo ziphaso zina monga pasipoti, layisensi ya galimoto kapenanso kalata ya kwa amfumu ngati momwe zinkakhalira mmbuyomu, sipakadakhala zokokanakokana ayi,” adatero a Maluwa.
Koma mu yankho lomwe wapampando wa bungwe la MEC mayi Annabel Mtalimanja akhala akupereka ku zipani ndi mabungwe ndi loti bungwelo likuyendetsa chisankho motsatira zomwe malamulo amanena.
Gawo 4 (3) loyendetsera chisankho cha pulezidenti, aphungu ndi makhansala limapereka chilolezo ku MEC chopangitsa kalembera wa chisankho kwa masiku osaposa 14 koma chibwereza chidabweramo kaamba ka chigamulo chaku khothi choti mmalo onse a kalembera mukhalenso a NRB.