Aotcha makilogalamu a chamba
Bwalo la milandu ku Salima lagamula kutentha chamba chokwana makilogalamu 576.68 komanso kuti mwini wake, a Adam Likagwa a zaka 34 apereke chindapusa cha K2 miliyoni kapena akaseweze ndende kwa miyezi 12.
Apolisi adamanga a Likagwa pa 22 March pomwe adadzadzitsa chambachi m’galimoto ya mtundu wa Toyota Sienta ndipo adalibe chitupa cha chololeza kuti iwo apezeke ndi katunduyu.

Mneneri wa polisi ya Salima mayi Rabecca Ndiwate ati a Likagwa adalephera kupereka ndi kuonetsa umboni wa chitupa cha chilolezo ku bwalo la mlandu kuti iwo apezeke ndi chambachi, ndipo woimira boma pa mlandu mayi Ida Mzama adapempha bwalo kuti lipereke gamulo lokhwima.
Ndipo a Likagwa adauvomera mlanduwo, koma adapempha chikhululuko poti iwo ali ndi banja.
Popereka gamulo, wozenga mlanduwu a Anthony Banda adagwirizana ndi ganizo la boma kupereka gamulo lokhwima, choncho adagamula a Likagwa kuti apereke chindapusa chokwana K2 miliyoni kapena akaseweze ndende kwa miyezi 12.
Adama Likagwa amachokera m’mudzi mwa Kambadi, T/A Nsamala, ku Balaka.