Nkhani

Kampeni yayamba ndi ukali

Listen to this article
  • DPP ithamangitsa otsutsa ku Thyolo
  • Kumeneko ndi kunyumba kwa APM—Chakale

Kwa eni kulibe mkuwe. Mdima udadza masanasana m’boma la Thyolo pamene gulu la Chilima Movement lidalephera kuchititsa msonkhano wake nkhondo ya mawu itabuka ndi otsatira chipani cha DPP.

Kaliati: Adatchinga msewu

Wachiwiri kwa mlembi wa DPP, Zelia Chakale, adati gulu la Chilima Movement lidachita kuishosha dala chifukwa limafuna kuchititsa msonkhano kunyumba kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.

“Thyolo ndi kunyumba kwa pulezidenti [Peter Mutharika]. Ndiye amafuna apite kumeneko kuti aziti atithamangitsako?” anadabwa Chakale.

Malinga ndi mneneri wa gulu la Chilima Movement, Patricia Kaliati izi zidachitika Loweruka pamene amafuna kuchititsa msonkhano wotsatsa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima.

Msonkhanowo umayembekezereka kuchitika ku Mapanga m’boma la Thyolo lomwe ndi dera la phungu wa DPP komanso gavanala ku chigawo chakummwera Charles Mchacha.

“Titadutsa pa Thunga n’kuyandikira Mapanga, tidaona anyamata a DPP atatchinga msewu, adaika miyala komwe timalowera, sitikadachitira mwina koma kubwerera chifukwa amafunanso alande zida zathu,” adatero Kaliati.

Chakale: A Chilima Movement anayishosha dala

Sabata yatha anyamata a DPP akutinso adavula anthu amene adavala malaya a makaka a chipani cha PP ndi MCP m’bomalo.

Naye wachiwiri kwa mtsogoleri wa MCP Sidik Mia, apolisi adamuthira utsi wokhetsa misonzi pamene amayendera gulu la achinyamata ku msika wa Blantyre.

Mneneri wa MCP Maurice Munthali adati ndi wokhudzidwa ndi nkhanizi chifukwa zitha kubala zisankho zoipa chaka chamawa.

“Tikufuna amene akukhudzidwa ndi zimenezi ayankhe. Ngati sipakhala kusintha momwe zikuchitikiramu, ndiye tipita kukhoti. Apolisi akuonetsa kuti akugwiritsidwa ntchito ndi chipani cha DPP,”adatero Munthali.

Komishona wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), Moffat Banda, adati n’zomvetsa chisoni kuti izi zikuchitika nthawi ya misonkhano yokopa anthu isadayambe.

“Makampeni awa ife sitikuwadziwa chifukwa ndikulakwa kuchititsa misonkhano ya ndale nthawi yake isadafike.

“Ngakhalebe nthawi ya kampeni sidayambe komabe sitifuna ziwawa zilizonse za ndale. Izi zingapangitse kuti Malawi akhale wamoto chifukwa zimayamba ndi zinthu zing’onozing’ono ngati izizi,” adatero Banda.

Kodi izi zingabale zisankho zotani?

Kadaulo wa ndale, Mustapha Hussein, adati zoterezi zikapitirira ndiye kuti zisankho za chaka cha mawa zitha kudzakhala za ziwawa.

“Izi zikuchitikazi zitha kubala zisankho zoipa. Vuto ndi loti zipani sizikulolerana. Komanso n’chifukwa chiyani DPP ikuti Thyolo ndi dera lokhalo la mtsogoleri wa dziko lino? Aliyense ali ndi ufulu wochititsa msonkhano malo amene akufuna,” adatero.

Mneneri wapolisi m’dziko muno James Kadadzera adati apolisi satenga mbali pandale.

Mkuluyu wapempha zipani zandale kuti zitsatira ndondomeko zoyenera pochititsa misonkhano pofuna kupewa ziwawa.

Kadadzera adakana kuti apolisi akugwiritsidwa ntchito ndi chipani cha DPP. “Aliyense akukhala ndi maganizo otere, koma dziwani kuti chipani chilichonse chikuyenera kutsatira ndondomeko zoyenera pochititsa misonkhano.”

Dziko la Malawi, lichititsa chisankho chapatatu m’mwezi wa May chaka cha mawa.

Pachisankhochi Amalawi adzasankha mtsogoleri wa dziko, aphungu a Nyumba ya Malamulo ndi makhansala.

Maiko monga Zambia, Zimbabwe, Ivory Coast ndi Gambia akhala pa ukapolo chifukwa cha ziwawa zomwe zimadza chifukwa chosemphana maganizo, komanso kusalorerana pandale.

 

Related Articles

Back to top button
Translate »