Kota yatha, JC yabwerera
Unduna wa za maphunziro wathetsa njira yosankhira ophunzira m’sukulu zaukachenjede yotchedwa kota, komanso yabwezeretsa mayeso a JC m’sukulu za sekondale.
Kudzera mu njira ya kota, yomwe yakhala ikudzetsa mpungwepungwe m’dziko muno, ophunzira amasankhidwa potengera boma lomwe amachokera osati momwe akhonzera.
Anthu ndi akatswiri azamaphunziro ayamikira boma chifukwa cha kusinthaku, koma achenjeza kuti boma lisachite izi pofuna kukopa anthu kudzavotera chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chidzachitike pa May 19 chaka chino.
Polengeza nkhaniyi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe Lachinayi, nduna ya maphunziro William Susuwere Banda idati boma lamvera maganizo a anthu, komanso malo m’sukulu zaukachenjede za boma achuluka poyerekeza ndi momwe zidaliri mmbuyomu.
“Monga mukudziwa boma lawonjezera malo m’sukulu zake. Kupatula apo, sukulu zina zomwe zidali pansi pa University of Malawi zaima pazokha zomwe zachititsa kuti malo achuluke m’sukuluzo.
“Boma lamvera Amalawi kaamba koti akhala akudandaula ndi njira ya kota, komanso kuchotsedwa kwa mayeso a JC,” adatero Banda.
Zipani zotsutsa boma zakhala zikugwiritsa ntchito kota pa kampeni ya chisankho cha pa May 19 2020. Mwachitsanzo, Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM akhala akuuza Amalawi kuti adzathetsa kota zikadzalowa m’boma.
Sinodi ya Livingstonia ya mpingo wa CCAP, yomwenso yakhala ikudzudzula boma chifukwa cha kota, yati siikambapo kanthu pokhapokha itaona kuti zinthu zasinthadi.
“Tamva koma sitinenapo zambiri chifukwa ilo ndi lonjezo chabe. Tiyambe kaye taona zikuchitika ndiye tidzalankhulapo,” adatero mlembi wamkulu wa sinodiyo Mbusa Levi Nyondo.
Wapampando wa gulu lina lotchedwa Quota Must Fall, lomwe lakhala likutsutsana ndi njirayi Dr Bina Shaba adati sakufuna malonjezo koma kuchotseratu kota.
“Tidzaomba m’manja tikadzaona zinthu zitasintha, koma padakali pano sitisiya kulankhula zotsutsana ndi kota,” adatero Shaba.
Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe loona zaufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC), Charles Kajoloweka, adati akhala akulondola ngati boma likuchitadi zomwe lalonjezazo.
“Lonjezo limakhala la phindu likakwaniritsidwa. Tamva koma tikhala tikulondolo n’cholinga chofuna kudziwa ngati boma likuchita zomwe lalonjezazo,” adatero Kajoloweka.
Mkulu wa bungwe Civic Society Education Coalition (Csec) Benedicto Kondowe adati nkhaniyi ndi yabwino, koma boma lisakhale likusewera ndi maganizo a Amalawi pogwiritsa ntchito kota ngati nyambo yokolera mavoti.
“Kuthetsa kota ndi ganizo labwino, koma tisalankhule zambiri chifukwa itha kukhala kampeni chabe.
“Nthawi zina boma limalankhula zinthu mongofuna kukopa anthu. Takhala tikulira za nkhanizi kwa nthawi yayitali ndiye lero lokha kwatani?” adafunsa Kondowe.
Mtsogoleri wa bungwe la sukulu zomwe si zaboma la Independent Schools Association of Malawi (Isama) Peter Patel wayamikira boma pobwezeretsa mayeso a JC.
Patel adati kuchotsa kwa JC kumalowetsa pansi maphunziro.
“Chomwe chimachitika n’choti ophunzira amangosewera kuyambira Folomu 1 mpaka Folomu 3 n’kudzadzidzimuka ali Folomu 4 chaka chawo cha mayeso ndiye amakhala kakasi chifukwa ntchito imachuluka zotsatira zake, ophunzira ambiri amalephera,” adatero Patel.
Pakati pa 2015 pomwe boma limathetsa JCE ndi 2019, ana 58 pa 100 aliwonse ndiwo amakhoza mayeso a MSCE pomwe pakati pa 2011 ndi 2014 JCE isadathe, ana 53 pa 100 aliwonse ndiwo amakhoza MSCE.
Koma Kondowe adati izo zilibe ntchito chifukwa kupanda kuthetsa JCE, bwenzi ana akukhoza kwambiri kuposa 58 pa 100 aliwonse potengera ndi momwe ndondomeko ya maphunziro idasinthira.
Makhozedwe pa zaka 8 adali motere: 2011 (51.8%), 2012 (51.8%), 2013 (52.48%), 2014 (54.08%), 2016 (58.32%), 2017 (61.66%), 2018 (63.00%) ndipo 2019 (50.36%).
Boma lidalengeza kuti lathetsa mayeso a JC mu September 2015 ndipo izi zidatanthauza kuti ophunzira akapita ku sekondale, azingokhulula mpaka Folomu 4 komwe amalemba mayeso aboma a MSCE.
Poteteza ganizolo, boma lidati iyi ndi njira imodzi yotetezera ndalama za boma chifukwa zimatanthauza kuti kuyambira Sitandade 1 ku pulayimale mpaka Folomu 4 ku sekondale, ophunzira azilemba mayeso aboma awiri basi a Sitandade 8 (PSLC) ndi pa MSCE.
Njira ya kota idayamba m’chaka cha 1987, koma anthu akhala akuikana koma boma limakakamirabe kuigwiritsa ntchito.