Nkhani

Mtsutso pa masiku a chisankho

Listen to this article

Mtsutso wabuka pa za masiku a chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chikuyembezeka kuchitika pa May 19 chaka chino.

Pamene ena akuti masiku ndi okwanira, ena akutsutsa kaamba koti chisankho chimalira zambiri.

Jane Ansah: Mtsogoleri wa MEC

Chisankhochi chikuyenera kuchitika pa  May 19 2020 potsatira chigamulo cha khothi choti chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chichitikenso m’masiku 150 kuchokera pa February 3 2020 litapeza kuti chisankho cha pa May 21 2019 sichidaye bwino.

Katswiri wa ndale George Phiri wati masikuwa ndiwokwana kuchititsa chisankho.

“Kupanda kupanga chisankho m’masikuwa ndiye kunyozera chigamulo cha khoti.

“Chofunika n’kusankha akuluakulu oyendetsa zisankho m’masiku 10 akudzawa pambuyo pake kuchititsa kalembera m’masiku 30 kwinako n’kosavuta chifukwa zambiri anthu akuzidziwa kale,” adatero Phiri.

Koma mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Justice Network (Mesn) Steve Duwa adati masiku 78 ndiosakwanira.

 “Bungwe loyendetsa zisankho likuyenera kukhala ndi akuluakulu atsopano, komanso pali ndondomeko zina zomwe ziyenera kutsatidwa,” watero Duwa.

Komiti ya ku Nyumba ya Malamulo yoona zosankha anthu m’maudindo ena a m’boma ya Public Appointments Committee (PAC) idapempha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti achotse ntchito akuluakulu a Malawi Electoral Commission (MEC) omwe adayendetsa zisankho za pa May 21 2019 kaamba koti adasokoneza zinthu.

MEC idapepha khoti kuti lionjezere masiku ochititsa zisankho, koma lidakana.

Related Articles

Back to top button
Translate »