Nkhani

Nanga wapolisi ataphofomoka?

Masiku ano sichikhala chachilendo kuona apolisi atakwera galimoto mosayenera. Ngakhale ntchito yawo n’kuonetsetsa kuti malamulo akutsatidwa, ngakhale pamsewu, apolisiwo ndiwo amakhala oyamba kuphwanya malamulowo. Kodi anthu wamba atakwera galimoto monga achitira apa apolisi, sangakalowe kozizira? Mwinatu iwowa ali ndi mphamvu kuposa lamulo.

Uku kudali kumpira wa Malawi ndi Kenya Lachitatu ku Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre. Chomwe chimadabwitsa n’chakuti nanga ataphofomoka pa galimotoyo, olakwa akuwathamangitsawo angagwidwe ndi ndani?

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button