Nkhani

Wa zaka 70 wofuna kugwiririra amangidwa

Listen to this article

Bwalo lamilandu la Dedza Lachiwiri lagamula gogo wa zaka 70 kuti akaseweze kundende zaka zinayi kaamba kofuna kugwiririra mdzukulu wake wa zaka 10.

Mneneri wa polisi ya Dedza, Edward Kabango, wati bwaloli lamva kuti gogoyu Falaviyasi Flytone pa 4 June adanyengerera mdzukulu wake yemwe ali sitandede 5 kuti amutsatire kudimba komwe amati akamuthyolere ndiwo.

Kabango wati awiriwa atafika kudimbako adamuthyolera mzimbe mwanayu kuti abaseweretsa mano iye akuthyola masambawo.

Iye wati mosakhalitsa gogoyo adasiya za masambazo ndi kumbwandira mwanayo. “Apa adayamba kumuvula zovala. Padali kulimbana chifukwa mwanayo samadziwa chomwe bambowo amafuna,” adatero mneneriyu.

Mkulu wina yemwe adali mboni ya boma m’bwalolo, Maxwell Chambu, wa m’mudzi mwa Kadzadza kwa T/A Kachere m’bomalo wati ndiye adawona izi zikuchitika.

Chambu polankhula ndi Msangulutso wati iye amadutsa mphepete mwa dimbalo kotero adafuna akhotere pathengo loyandikana ndi dimbalo kuti asambe.

“Pafupi ndi dimbalo pali madzi, ndiye poti ndikhote ndidamva mtswatswa, nditayang’ana ndipomwe ndidawona mkuluyu. Ndidabwerera changu poganiza kuti akudzithandiza.

“Pobwererapo ndidaponda chitsamba chouma ndiye iye adadzambatuka ndi mwana yemweyo. Apo n’kuti ali ndi buluku m’manja pomwe mwanayo adali mbulanda,” adatero Chambu.

Chambu wati adathamangira pambutopo ndipo adafunsa gogoyu zomwe amachita ndi mwanayo koma iye adadziluma.

“Mwanayo adafotokoza kuti gogoyo adamumbwandira kuti amugone. Iye adati poyamba samadziwa chomwe gogoyo amafuna amuchite koma adangodabwa watulutsa maliseche ake kuti athane ndi mwanayo.

 

“Iye adati atamuvula mwanayo adalimbalimba kuti asathe kumuvula kabudula wa mkati koma gogoyu akuti adangomung’amba,” adatero Chambu yemwe adatenga mwanayo ulendo kumudzi.

Mkuluyo akuti adagwidwa ndi usiku wa tsiku lomwelo.

Koma Kabango wati nkhaniyi italowa m’bwalo woweruza mlandu Damiano Chibwana sadachedwe koma kulamula kuti gogoyu akaseweze zaka zinayi kundende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga.

“Iye adati pachipanda kuwapezerera bwezi atagona ndi mwanayu chifukwa adawapeza atachotsa kale zovala ndiponso ali pamwamba pa mwanayu,” adawonjeza Kabango.

Gogoyu anadandaulira bwalo kuti limufewetsere chilango ponena kuti ndi wokalamba koma woweruzayo adati ili likhale phunziro kwa ena.

Gogoyu ndi wa m’mudzi mwa Mbidzi kwa T/A Kaphuka m’bomalo.

Related Articles

One Comment

  1. amufewetserechilango chifukwa ndi wokalamba koma asazayambirenso chifukwa mahule ndiwochuluka

Back to top button