Nkhani

Nkhanza zankitsa

Kodi n’chiyani Amalawi? Sabata yadutsayi, yakhala yowawa pomwe anthu apalamula milandu yoopsa, yosamvetsetseka.

M’sabatayi, bambo wina wa zaka 24, yemwe amakhala m’dziko la South Africa, ndipo adasiya bwenzi lake ku Manyamula m’boma la Mzimba, adabwera m’dziko muno ndi cholinga chodzapha bwenzi lakelo.

Nkhani zogwirira ana, amayi zayala nthenje

Malinga ndi mneneri wa apolisi m’boma la Mzimba, Peter Botha, apolisi akuganizira kuti Emmanuel Mizwa adamubaya katatu Annie Nkhoswe wa zaka 18 yemwe adamupeza kumjingo akutunga madzi.

Ndipo lipoti lomwe apolisi atulutsa pankhaniyi likuti Mizwa yemwe amachokera m’mudzi mwa Chipasula, kwa Inkosi ya Makhosi Mmbelwa V, m’bomalo adamupha Nkhoswe chifukwa adathetsa ubwenzi wawo ndi kugwa m’chikondi ndi mwamuna wina.

Lipotilo lati Nkhoswe adafera pomwepo pomwe Mizwa adatsekeredwa ndipo pakadalipano akadali m’manja mwa apolisi.

Dziko lino lidadzidzimukanso Lachiwiri lomwelo pomwe bambo wina wa zaka 38 yemwe amagwira ntchito kukampani yopanga shuga ya Illovo adagwiririra mwana wa zaka 11 ku Mulomba, m’bomalo.

Kanema wa mwanayu yemwe adali magazi okha okha idazungulira m’masamba a mchezo.

Malinga ndi lipoti lomwe apolisi adatulutsa pankhaniyo, Renald Kanyama akumuganizira kuti adagwiririra mwanayo pomwe adachoka ku nyumba kwa bambo wake, m’mudzi wina osawadziwitsa ndipo ankapita ku Nchalo kukayang’ana mayi wake.

Panthawiyi n’kuti bamboyo yemwe amakhala ndi mkazi wake wachiwiri, adali atachoka pakhomopo m’mawa wa tsikulo pamodzi ndi mkazi wakeyo.

“Panjira adakumana ndi Kanyama yemwe adali panjinga ndipo adamunyamulako mwanayo. Koma atafika patchire lina, adamugwirira,” latero lipotilo.

Pakadalipano, mwanayo yemwe ali mu Sitandade 3 pasukulu ina akulandira thandizo la mankhwala pachipatala cha boma ku Chikwawa.

Malinga ndi Wezzie Moyo, mmodzi mwa akadaulo woona  nkhani zoti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito, wati milandu ya mtunduwu iyenera kuyendetsedwa msanga.

“Mwana anagwiriridwayo ayenera kuthandizidwa maganizidwe chifukwa izi zikhonza kumusokoneza moyo wake onse.

Makhoti asamachedwe kuzenga milandu yotere komanso kupereka chilango chogwirizana ndi mlanduwo. Komanso boma lichilimike pofuna kuonetsetsa kuti ndalama zothandizira kulimbana ndi nkhanza kwa amayi zikhale zopezekeratu.

Izo zili apo anthu ena olusa adatentha malo ofikira alendo omwe ali pafupi ndi nyumba ya boma mzinda wa Lilongwe a Kumbali pa mkangano wa malo mkati mwa sabatayi.

Galimoto 7 komanso nyumba zitatu zogona alendo ndi sukulu ya mkombaphala zidapsa ndi motowo.

Ndipo gogo wina Stella Chigule adaphedwa m’boma la Dedza pomuganizira kuti ndi thakati.

Ndipo mayi wina ku Chirimba, Ivy Mutawira, padakalipano wakamang’ala kumabungwe chifukwa apolisi awiri, omwe akuoneka kuti adalawa, adamumenya molapitsa pomwe amasaka mwamuna wake.

Mutawira, padakali pano akulephera kuona apolisiwo atamumenya pa 4 September pomwe amafuna kumugwirira atamanga mwamuna wakeyo cha m’ma 7 koloko usiku. Iye akuona kuti apolisi sakumuthandiza atalembera mkulu wa apolisi George Kainja.

Komatu nkhani zoziziritsa thupizi sizidathere pompa chifukwa nawo apolisi mumzinda wa Blantyre, akusunga m’chitokosi Mike Mphuka wa zaka 46, mkazi wake Catherine Mphuka wa zaka 48 atapezeka atafa m’nyumba mwawo koma alibe minofu ina ya nkhope yake.

Malinga ndi mneneri wa polisi ku Blantyre, Augustus Nkhwazi, bamboyo adasiya mkazi wake kunyumba Lachiwiri pa October 20, ndi mwana wawo wa zaka 8.

“Koma pobwera adapeza mkazi wakeyo atafa koma alibe minofu ina monga m’masaya, mlomo wa m’munsi, khutu limodzi komanso pachipumi,” adalongosola Nkhwazi.

Ndipo iye adati, pomwe thupili adalitengera pachipatala cha Gulupu mumzinda wa Blantyre, adapeza kuti mayiyu adafa chifukwa chovulazidwa.

Polankhulapo m’Nyumba ya Malamulo, mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera adadzudzula kwatunthu mchitidwe wophana komanso wotengera malamulo m’manja omwe anthu akuchita m’dziko muno.

Chakwera adatsimikizira amayi ndi achikulire onse m’dziko muno kuti boma lake liwateteza.

Mphunzitsi wa za chitetezo pasukulu ya ukachenjede ya Mzuzu University (Mzuni) Euginio Njoloma adati moyo wa uchigawenga, nkhanza komanso upandu ukunka nukula m’dziko muno kusiyana ndi zaka za mmbuyo.

Njoloma adati pali zifukwa zingapo zomwe zikhonza kukhala kuti zikukolezera mchitidwewu monga kusunga mikwiyo chifukwa cha mavuto komanso kupezerera anthu opanda mphamvu monga anthu achikulire ndi ana.

Iye adatinso anthuwanso akutengerapo danga lochitira nkhanza ana ndi achikulire chifukwa ambiri mwa anthuwa alibe owateteza

“Tisangodalira apolisi okha, koma tonse titengepo gawo loteteza anthuwa,” iye adatero.

Related Articles

Back to top button