Nkhani

Tikumafa nthawi ya chisankho achialubino adandaula

Anthu ambiri m’dziko muno akugwedezabe mitu ndi nkhani yomwe inachitika ku Kasungu.

Kumeneko, apolisi anamanga mayi wina yemwe amachokera m’mudzi mwa Chinkhombwe ku dera la mfumu Chakhaza ku Dowa koma amakhala ku Kasungu m’mudzi mwa Chisazima kaamba ka kuphedwa kwa ana anayi.

A Muhamba: Titetezeni

Nkhani yomwe yadabwitsa si kuphedwa kwa anawawo, koma m’mene anaphedwera.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomalo a Joseph Kachikho, anawa, omwe ndi Richard Nkhata wa zaka 8 ndi Samson Nkhata wa zaka zinayi a m’mudzi mwa Masaka mfumu Chinyama, Kelvin Banda wam’mudzi mwa Sangala kwamfumu Suza komanso Funny Banda wa chaka chimodzi ndi miyezi isanu am’mudzi mwa Makanda kwamfumu Mwase ku Kasungu komweko, samapeza bwino.

Makolo a anawa anapita nawo kwa mneneri wina wake wa zaka zinayi yemwe ndi mwana wa mayi wamangidwayo kuti mwina n’kukachira kudzera ku mizimu.

A Chikumbu: Ndinadandaula

Atafika kwa mneneriyo, anauza amayi ake kuti awakwapule anawo ndi mtengo. Anawo anakwapulidwa kwambiri

A Magombo: Akuyenera kuwapima

Bungwe la achialubino la Association of People Living with Albinism in Malawi (Apam) lati likuda nkhawa ndi chisankho chikubwerachi chifukwa ndi nthawi yomwe amachitiridwa nkhanza kapena kuphedwa kumene.

Mkulu wa bungweli a Young Muhamba ndiwo adandaula izi poyankhapo pa nkhani ya manda a munthu wachialubino omwe anafukulidwa ku Mulanje.

Apolisi m’boma la Mulanje akufunafuna anthu womwe anafukula manda a munthu wachialubinoyu.

Malingana ndi mneneri wapolisi m’bomalo a Innocent Moses, izi zinachitika m’mudzi mwa Chinomba ku dera la mfumu Chikumbu.

A Muhamba anati palibe chodabwitsa pa nkhaniyi, makamaka nthawi ya chisankho ikamayandikira.

“Nkhawa yanga ndiyoti nkhani za kuvulaza, kupha kapena kufukula manda a anthu achialubino sizikutha m’dziko muno. Nthawi zambiri apolisi akhala akuchita zinthu mochedwa, makamaka pa nkhani yomanga anthu ankhanzawa.

“Tikuwapempha kuti afufuze nkhaniyi ndi kumanga omwe akuchita izi. Pali chizolowezi choti zisankho zikayandikira, khalidwe lochitira nkhanza anthu achialubino likumakula. Kodi tilowera kuti?” Iwo anadandaula.

Mfumu Chikumbu inati inadandaula kwambiri itamva zoti m’dera lawo mwachitika zimenezo zomwe inati zikumachitika ndi anthu osakonda anzawo komanso opanda umunthu.

Mfumuyi inapemphanso apolisi kuti afufuze mwachangu nkhaniyo kuti omwe achita izi agwidwe.

A Moses anati apolisi m’bomalo ali pa kalikiliki kusaka achiwembuwo. Iwo anapempha anthu kuti azikanena kupolisi ngati akuganizira anthu ena.

Pa nkhani ya chitetezo cha anthu achialubino, mneneri wapolisi m’dziko muno a Peter Kalaya anati mavuto omwe anthu achialubino akukumana nawo akuwadziwa bwino.

“Choncho tikuwatsimikizira kuti tichita chilichonse chotheka kuteteza miyoyo m’mutu chimene chinachititsa kuti amwalire.

Kodi mwana wa zaka zinayi angauze mayi ake chochita ngati chimenechi? Kapena ndi mphamvu ya Mulungu?

Mtsogoleri wa mpingo wa Charismatic Redeemed Ministries International a Mark Kambalazaza akana. Iwo anati akudabwa komwe mwanayo anatenga mphamvu imeneyi.

“Zoti mwana wa zaka zinayi angakulamule chochita ndikukaika. Komanso dziwani kuti palibe nthawi imene Yesu anachilitsa munthu kudzera m’kumenya,” iwo anatero.

A Kambalazaza anati mavuto ngati amenewa amabwera kaamba ka kusawerenga Mawu a Mulungu chifukwa anati Yesu ananena poyera kuti anthu adzitsata zomwe amachita.

Katswiri pa kaganiziridwe (psychologist) a Beatrice Magombo anati sichinthu chabwino kukhulupirira zomwe mwana walankhula kuposa wamkulu.

“Ndibwinonso kufufuza kapena kuyeza mwanayo kuti adziwe ngati ali bwino kapena pali kusokonekera kwina kwake,” iwo anatero.

A Magombo anadzudzulanso mchitidwe wopita ndi ana kwa aneneri m’malo mwa koyenelera kuti akalandire thandizo. “Kunena zoona, kumeenya ana mpaka kupha ndi nkhanza zazikulu. Koma chofunika n’kupima mwanayo ndi makolo ake ngati ali bwino kapena ayi,” iwo anatero.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button