2021: Chaka cha kukwera kwa katundu
Chaka cha 2021 chidali chaka cha kwera nane nkwereko wakatundu, makamaka yemwe Amalawi amadalira kwambiri pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku.
Kumayambiliro a chakachi, Amalawi amadandaula kuti akapita kokagula katundu monga mafuta ophikira, mchere, shuga kapena sopo ku golosale, amakapeza mtengo watsopano nthawi zonse.
Mtengo wa mafuta ophikira ndiwo udanyanya panthawiyo chifukwa botolo la malita 5 lomwe linkagulidwa pa mtengo wa K4 500 lidakwera mpaka kufika pa K11 000.
Koma makampani opanga mafutawo adakankhira vutoli ku boma ponena kuti misonkho yomwe lidakhazikitsa pa mafuta ndiyokwera kwambiri.
Katundu osiyanasiyana akukwerabe chomwecho, a Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) nawo adalengeza kuti mtengo wamafuta a galimoto wakwera.
M’mwezi wa October 2021, Petulo adakwera kuchoka pa K899.2 kufika pa K1 150, diziro kuchoka pa K898 kufika pa K1 120 pomwe parafini adachoka pa 719.60 kufika pa K833.20.
Polongosola kukwerako, bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) lidati yatsatira momwe mitengo yamafuta ikuyendera padziko lapansi.
“Mtengo wamafuta wakwera dziko lonse lapansi komanso ifeyo tatenga nthawi osakweza ndipo zafikapa palibe kuchitira mwina,” idatero kalata yomwe Mera idatulutsa nthawiyo.
Koma pa nyengo ngati yomweyo, ku Zambia petulo adali pa K875.30 pomwe diziro adali pa K774.46. Ku Tanzania, petulo adali pa K865.95 pomwe diziro adali pa K803.16. Ku Zimbabwe petulo adali pa K1 138.25 pomwe diziro adali pa K1 106.82. Ku South Africa petolo adali pa K1 014.69 pomwe diziro adali K857 ndipo ku Kenya petulool adali pa K1 005.81 pomwe diziro adali pa K863.06.
Pamene kubuula kwa kukweraku kudali mkati, magetsi ndi madzi zidakweranso pafupifupi nthawi imodzi ndipo zitafika apa, Amalawi adayamba kuchita zionetsero zotsutsana ndi kukwera kwa katunduyo.
M’modzi mwa omwe akhala akutsogolera zionetserozo a Bon Kalindo adati boma lasempha msewu ndipo likulowera kolakwika chifukwa m’malo mokwaniritsa malonjezo, atsogeleri akuonelera Amalawi akulira.
“Ifeyotu tikufuna atsitse mitengo yakatundu chifukwa omwe akumva kuwawa ndi Amalawi omwe adakavota kusankha atsogoleriwo pokhutira ndi malonjezo awo. Koma lero ayang’ana kumbali,” adatero a Kalindo.
A Silvestre Namiwa a bungwe la Centre for Democracy and Economic Development Initiative (Cdedi) nawo adati boma la Tonse Alliance lidanamiza Amalawi n’chifukwa chake adayamba kupanga zionetsero.
“Ngati mukukumbuka bwino, ankaima pansanja n’kumatiwuza kuti fetereza tidzagula pa mtengo wa K4 500, koma lero wafika pa K38 000,” adatero a Namiwa.
Mkulu wa bungwe loimira ogula ndi kugwiritsa ntchito katundu a John Kapito adati ngakhale mafuta adakwera dziko lonse, boma limafunika ndondomeko yokwezera mtengo pang’onopang’ono osati kamodzi.
“Si mafuta okha ayi ngakhale katundu wina sadakwere bwino poyerekeza ndi nyengo yomwe tikudutsamoyi,” adatero a Kapito.
Mtsogoleri wambali yotsutsa boma mu Nyumba ya Malamulo a Kondwani Nankhumwa adadzudzula boma pa nkhani ya kukwera kwa mtengo wakatundu.
“Sindikukhulupilira kuti tikulowera ku Kanani tinkalonjezedwa kuja. Amalawi akukumana ndi zowawa, makamaka pa kukwera kwa mtengo wakatundu,” adatero a Nakhumwa.
Muuthenga wake, mtsogoleri wadziko lino a Lazarus Chakwera adati akudziwa kuti Amalawi akudutsa m’zowawa. Koma iwo adati mpofunika kupilira chifukwa mavutowa ndi njira chabe ya kuchimwemwe.
Mneneri waboma a Gospel Kazako omwenso ndi nduna ya zofalitsa nkhani adati boma likukonza zinthu pang’onopang’ono moti zina zizitheka mwachangu pomwe zina n’zofunika nthawi.
“AMalawi adekhe zonse sizingatheke nthawi imodzi. Pali zina zomwe tayamba kale kukonza, koma anthu ayenera kuvomereza kuti pali zina zosatheka kupanga pompopompo,” adatero a Kazako.