Nkhani

Apolisi azilembanso mayeso a malamulo

Listen to this article

Patadutsa zaka 20 apolisi asakulemba mayeso okhudza zomwe malamulo a ntchito yawo amanena omwe m’Chingerezi amatchedwa Service Standing Order (SSO), apolisiwa ayamba kuwalembanso.

Izi zikutanthauza kuti apolisi omwe adalembedwa kuchokera m’chaka cha 2001, sadalembepo mayesowa omwe amafunika kulembedwa chaka ndi chaka.

Apolisi sayenera kuiwala malamulo a ntchito yawo

Mayesowa, ntchito yake n’kukumbutsa apolisi za ndondomeko za kagwiridwe ka ntchito yawo ndipo amafunika kuti aziwerenga bukulo pafupipafupi.

Mwa zina, malamulowa amalongosola za kafufuzidwe ka mlandu komanso kagwiritsidwe ntchito ka mfuti.

Malamulowa, amaletsanso apolisi a pabanja kuchita chibwenzi ndi mwana wa apolisi anzawo kapena m’polisi mnzawo. Potengera malamulowa, wapolisi wopezeka akuchita izi amaimbidwa mlandu m’ndondomeko yawo.

Malamulowa amatinso wapolisi aliyense akakwatira, akuyenera kupititsa kwa akuluakulu ake setifiketi ya ukwati komanso ngati adalekana ndi wokondedwa wake akuyenera apereke kupolisiko setifiketi yochokera kukhoti yotsimikiza kuti awiriwo adalekanadi.

Komatu n’zodandaulitsa kuti pakatipa apolisi ambiri amangochita madulira pa kagwiridwe kawo ka ntchito ndipo samatsatira mwachindunji ndondomeko zokhazikitsidwa mu SSO.

Mayesowa abwera pomwe mkulu wa apolisi m’dziko muno a George Kainja adalengeza kuti polisi yasintha khalidwe.

Kainja adanena izi Lachitatu pa 30 June kwa Msundwe m’boma la Lilongwe.

Polankhulapo, mneneri wa polisi m’dziko muno a James Kadadzera adati apolisi ayamba kulemba mayesowa mwezi watha.

“Nkhani yake siyongolemba mayesowa ndi kukhonza ayi. Koma kukumbukira ntchito ya polisi ndi kuti tizigwira mwa ukadaulo ndi kudziwa chomwe ukuyenera kuchita pogwira ntchito,” adalongosola a Kadadzera.

Iwo adati akuluakulu apolisi pano adaona kufunikira poyambitsanso mayesowa.

“Ambiri amaphonya pa kagwiridwe ka ntchito chifukwa bukuli sadaliwerenge. Koma akamalemba mayeso azikakamizika kuwerenga malamulowa,” iwo adatero.

A Kadazera adapereka chitsanzo choti bukuli lidapereka ndondomeko zonse za kagwiritsidwe ntchito ka mfuti apolisi akakumana ndi mikwingwirima yofunika mfuti.

“Sitikhalanso ndi nkhani zoti apolisi adapanga chidule ndipo milandu ngati iyi ichepa,” adalongosola iwo.

Potsilirapo mang’ombe, mphunzitsi pasukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia (Unilia) a George Phiri adayamikira apolisi poyambanso mayesowa.

Iwo adati anthu ambiri aphedwa m’manja mwa apolisi kuphatikizapo a Buleya Lule chifukwa apolisiwa sakudziwa ndondomeko zawo zogwirira ntchito.

“Nthawi zina apolisi amayambitsa chipwirikiti pamalo m’malo mosungitsa bata. Nthawi zina amangoombapo mfuti mwachisawawa mpaka kupha anthu,” adalongosola a Phiri.

Malinga ndi iwo, buku la malamulo apolisiwo likufunika liziunikidwanso pafupipafupi kuti lizigwirizana ndi kusintha kwa nyengo.

Related Articles

Back to top button