Nkhani

Mtengo wa chimanga wapenga

 Kusowa kwa chimanga m’misika ya Admarc kwapereka danga kwa mavenda ogulitsa chimangacho kuti akame Amalawi omwe akulira kale ndi njala pokweza mtengo wa chimangacho mopanda chisoni.

M’misika yambiri yomwe tazungulira, mavenda akugulitsa chimanga pa mtengo wosachepela K1 300 pa kilogalamu kutanthauza kuti thumba la makilogalamu 50 likugulitsidwa pa mtengo wosachepera K65 000.

Kugula chimanga ku Admarc ndi nkhondo. |

Apa zikutanthauza kuti ndalama zomwe zikadakwanira kugula matumba awiri a makilogalamu 50 lililonse pa mtengo omwe boma lidakhazikitsa wa K650 pa kilogalamu, zikugula thumba limodzi la makilogalamu 50 omwewo.

Pomwe boma linkakhazikitsa mitengo ya mbewu mu April 2024, mtengo wa chimanga udakhazikitsidwa pa K650 pa kilogalamu ngakhale kuti kaamba ka kuvuta kwa kakololedwe, mtengowo udayamba kukwera pang’onopang’ono mpaka kufika pa K790 pa kilogalamu.

Malingana ndi Amalawi ena omwe adacheza ndi Tamvani, izi zikuchitika chifukwa m’misika ya Admarc mulibe chimanga ndiye mavenda akudziwa kuti olo akwenze mtengo chotani, Amalawi agulabe chifukwa alibe kokatenga chakudya.

“Kukadakhala kuti ku Admarc kuli chimanga sizikadafika pamenepa chifukwa ku Admarc mtengo wa chimanga ndi womverera ndiye bwenzi anthu akuthamangira ku Admarc kenako mavenda nawo akadatsitsa mitengo yawo kuti bizinesi iziyenda,” adatero a Yamikani Jiya ku msika wa Nsungwi ku Lilongwe.

Mavenda akayamba kukweza mtengo wa chimanga mobera Amalawi, Admarc imatsegula misika yake n’kutumizamo chimanga chambiri kuti anthu azigula pa mtengo wotsika zomwe zimapangitsa kuti mavenda nawo atsitse mtengo wa chimanga chawo.

Koma mneneri wa Admarc mayi Teresa Chapulapula adati mwa misika 360 ya Admarc yomwe ili m’dziko muno, misika 331 idatsegulidwa kale

 koma kuti chimanga chambiri chikuchokera ku maboma a ku mpoto kupita m’madera ena monga kummwera.

“An t h u a k u y e n e r a kumvetsetsa kuti chaka chino, Admarc idagula chimanga chambiri m’chigawo cha ku mpoto ndiye chimangacho chikuyenera kusamutsidwa kuchoka kumpoto kukafika m’madera ena ngati ku mmwera,” adatero a Chapulapula.

Polingalira za njala yomwe yakhudza anthu pafupifupi 7.5 miliyoni m’dziko muno, nthambi ya boma yosunga chakudya ya National Food Reserve Agency (NFRA) idaika pamphepete chimanga chokwana matani 20 000 choti Admarc igulitse pa mtengo wotsika.

Koma mkulu wa NFRA a George Macheka ati mwa chimangacho, matani 5 000 okha ndiwo adaperekedwa kale ku Admarc ndipo matani ena 15 000 akadali ku nkhokwezo.

A Macheka ati chimangacho ndi chokwana kugawa m’misika yonse ya Admarc ndipo zitatero, ndiye kuti mitengo ya chimanga ikhoza kutsika chifukwa Admarc imagulitsa chimanga pa mtengo wovomerezeka ndi boma ndipo misika yake imapezeka paliponse.

“Chimanga chi l ipo, akuluakulu a nthambi yathu limodzi ndi komiti yoona za malonda a chimanga adakhazikitsa zoti mwa matani 106 000 a chimanga omwe tidagula, matani 20 000 tipereke ku Admarc kuti chithandize kukhazikitsa mtengo womverera wa chimanga. Padakalipano tidaperekako matani 5 000,” adatero a Macheka.

Wachiwiri kwa wapampando wa komiti ya za malimidwe ku Nyumba ya Malamulo a Ulemu Chilapondwa adatsimikiza kuti NFRA itatulutsa matani 5 000 kupita ku Admarc, mtengo wachimanga udatsika.

“Ndi zoona, pakati apo anthu mwina adangoona kuti mtengo wa chimanga wakhwefuka, chifukwa chidali choti chimangacho chidapezeka m’misika ya Admarc ndiye mavenda adatsitsa chawo kuti azipikisana ndi Admarc,” adatero a Chilapondwa.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Back to top button