America iyimika thandizo
Kadaulo wa mgwirizano wa mabungwe a zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) a George Jobe ati zomwe lachita dziko la America poimika thandizo kwa masiku 90 likhale phunziro ku dziko la Malawi.
A Jobe adanena izi mtsogoleri wa dziko la America a Donald Trump atalamula kuti nthambi ya bomalo yomwe imapereka thandizo ku maiko ena la USAid iimike kaye ntchito zake mpaka a Trump atakhutitsidwa ngati ntchito za nthambiyo zikugwirizana ndi maloto awo. USAid yakhala ikuthandi za dz iko l ino pa maphunziro, zaumoyo ndi ntchito zina za chitukuko.

Kuimika ntchito za USAid kukusonyeza kuti dziko lino silizilandira K493.7 biliyoni yomwe imathandiza mmagawo monga a zaumoyo, zamalimidwe, kulimbana ndi matenda a Edzi, maphunziro, za chilengedwe komanso uchembere wabwino.
“Apapa chofunika n’choti boma lipeze njira zotsekera momwe mwaloshoka msanga. America yapereka masiku 90 kuti iunikenso za thandizo lake ndipo sitikudziwa zotsatira za masiku 90 akunenawo. Ichi n’chifukwa chomwe timayenera kukha la okonzeka nthawi zonse,” atero a Jobe.
Mabungwe a za umoyo akhala akulimbikitsa boma kuti lizikwaniritsa mlozo wopereka K15 pa K100 iliyonse m’ndondomeko ya za chuma cha boma ku unduna wa za umoyo monga momwe maiko adagwi r i z i rana ku t i undunawo uzikhala ndi ndalama zokwanira zogwirira ntchito mmalo momadalira kwambiri thandizo la maiko ena.
Pa nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi, America imathandiza ndi K134.6 bi l iyoni, za umoyo zina K81.9 bi liyoni, za ulimi K53.7 biliyoni, maphunziro a pulaimale ndi sekondale K43.2 biliyoni, za uchembere wabwino K40.5 biliyoni, gozi zogwa mwadzidzidzi K19.5 biliyoni, boma ndi mabungwe oima pa okha K16.4 biliyoni, maphuziro odutsa sekondale K 14.7 biliyoni komanso za chilengedwe K13.2 biliyoni.
America ndi dziko lomwe limapereka thandizo lambiri ku maiko ena makamaka pa nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi kudzera ku thumba la President ’s Emergency Plan for Aids Relief (Pepfar).
Pa zomwe zachi t ikazi , mafumu akuluakulu ati ali ndi nkhawa kuti kuima kwa thandizolo kukhoza kukhudza anthu ambiri ndipo kukhoza kukhala chipere cha anthu omwe pakali pano akuyendera mankhwala otalikitsa moyo a ARV.
Mfumu yaikulu Salima ya m’boma la Salima yati anthu ambiri makamaka m’midzi amadalira thandizo lawulere la za umoyo kuphatikizapo omwe ali pa mankhwala otalikitsa moyo a ARV ndipo kuima kwa thandizolo n’chipsinjo kwa anthu oterowo.
“Zateremu tikuyang’anira ku boma chifukwa tikudziwa kuti sangalekerere kuti anthu apululuke chifukwa thandizo layima ayi, zililimu, okhawo omwe ali ndi ndalama kapena mabwana ndiwo ali ndi mpata wolandira thandizo loyenera la za umoyo,” atero a Salima.
Pomwe mfumu yaikulu Mwabulambia ku Chitipa yati kupatula chipere chomwe chingaoneke kaamba ka kusowa kwa thandizo la za umoyo, ntchito za ulimi nazo zili pa chiopsezo chifukwa mapulojekiti ambiri a za ulimi monga mthirira zimadaliranso thandizo lomwelo.
“Apapatu palibe poti tikhoza kuwiringula ayi chifukwa awowo ndalamazo ndi zawo. Chomwe timayenera ifeyo n’kumavula moyo wodalira pag ’onopang ’ono uku tikupanga dongosolo loti tizidzidalira. Mwachitsanzo, tikhoza kumapanga tokha zinthu ngati fetereza momwe anzathu ku Zambia akupangira,” atero a Mwabulambia.
Mfumu yaikulu Kawinga ku Machinga yati pakadakhala mpata woti n’kulankhula ndi boma la America, mafumu akadapempha mpata wotero kuti akafotokoze okha momwe anthu m’midzi amapindulira ndi thandizo la dzikolo n’cholinga choti lipitilire.
“Zi kungokha la ngat i kampeni ka nsengwa kuthwa konsekonse, uku ntchito za ulimi zisokonekere kwinaku za umoyo zisokonekerenso makamaka izi zokhudza matenda a Edzi zikutiopsa kwambiri chifukwa anthu ambiri akhoza kutisiya,” atero a Kawinga.
A Jobe ati koma b e chiyembekezo chikadalipo p o t i d z i ko la Amer i c a s i lida l engeze kusiy i ratu kupereka thandizo lodzera ku mabungwe ena monga la Global Fund omwenso amathandiza mmagawo ena monga za umoyo.