Nkhani

Anthu 500 000 sadalembetse

Zotsatira za kalembera wachisankho m’gawo loyamba ndi lachiwiri zasonyeza kuti anthu 468 860 omwe amayenera kulembetsa sadalembetse nawo m’kaundulayo.

Malingana ndi zotsatira zochokera ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), m’gawo loyamba, anthu 1 094 269 amayenera kulembetsa koma anthu 798 351 ndiwo adalembetsa kuimirira anthu 73 pa anthu 100 aliwonse.

M’gawo Lachiwiri, anthu 1 048 080 ndiwo amayenera kulembetsa koma anthu 875 138 okha ndiwo adalembetsa kuimirira anthu 83 pa anthu 100 aliwonse ofunika kulembetsa.

Apa zikutanthauza kuti m’magawo onse awiri, anthu 2142 349 ndiwo amayenera kulembetsa koma mmalo mwake, anthu 1 673 489 ndiwo adalembetsa kutanthauza kuti anthu otsala osalembetsa mmagawowa ndi 468 860.

Mwa anthu omwe adalembetsawa, 901 060 ndi amayi pomwe 771 922 ndi abambo ndipo chiwerengerochi sichidasangalatse chipani chachikulu chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) komanso bungwe lowona za ufulu wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR).

MCP ndi CHRR adapempha bungwe la MEC kuti liganizire kudzabwereza kalembera mmaboma omwe mudachitika kalemberayu mmagawo awiriwa kuti anthu omwe adatsalirawa adzapeze mpata wolembetsa.

Mneneri wa MCP Rev Maurice Munthali adati kalemberayo ngoyenera kuchitikanso m’maboma omwe adakhudzidwa chifukwa anthu omwe sadalembetse ndi wochuluka kwambiri.

“Sitingasiye anthu onsewa osalembetsa ayi ndiye kuti sitikudziwa chomwe tikupanga. MEC ikuyenera kudzabwerera mmaboma omwe akukhudzidwa mmagawo amenewa,” adatero Munthali.

Mkulu wa bungwe la CHRR Timothy Mtambo adati potengera kulemekeza ufulu wa anthu, mpoyenera kuti kalembera adzabwerezedwe mmaboma okhudzidwawa.

“Anthu ali ndi maufulu osiyanasiyana ndipo umodzi mwa maufuluwo ndi otenga nawo mbali posankha atsogoleri ngati momwe tikuyembekezera chaka cha mawachi. Apapa, zikuonetseratu kuti anthu ambiri sadalembetse kotero ufulu wawo odzasankha atsogoleri waphwanyidwa,” adatero Mtambo.

Mkulu wa MEC Jane Ansah adati kalembera m’magawo oyambirirawa adavuta chifukwa anthu adali asadamve mauthenga bwinobwino komanso padali mavuto okhudzana ndi zipangizo zomwe zimafaifa koma adati mavutowa adatha.

Iye adapempha mabungwe ndi zipani zandale kuti zichilimike kumema anthu kukalembetsa mkaundula kuti akavote nawo chaka cha mawa pachisankho cha patatu.

Mkulu wa bungwe loona kuti zisankho zikuyenda bwino la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adagwirizana ndi Ansah kuti mabungwe ndi zipani zandale athandizirepo kwambiri kumema anthu kukalembetsa kuti chisankho cha chaka chamawa chidzakhale chatanthauzo.

Related Articles

Back to top button