Nkhani

Adzudzula Admarc

Listen to this article

Mafumu ndi alimi ena m’zigawo zonse zitatu adandaula kuti msika wa Admarc watsegulidwa mochedwa iwo atagulitsa kale chimanga chawo motchipa kwa mavenda pofuna kuthana ndi mavuto a pakhomo.

Dandauloli ladza pomwe bungwe la Admarc Lolemba lidayamba kugula chimanga kwa alimi ang’onoang’ono pa mtengo wa K150 pa kilogalamu ndi kuti alimiwo apindule.

Alimi ena adagulitsa kale kwa mavenda

Koma mafumu ndi alimi ena atula nkhawa zoti mtengo wokhetsa dovuwu ukudza iwo alibe chimanga choti n’kugulitsa chifukwa chambiri adagula kale ma venda.

Inkosi Khosolo ya m’boma la Mzimba yati nzokaikitsa kuti alimi ang’onoang’ono akadali nacho chimanga choti n’kugulitsa ku Admarc poti ambiri amagulitsira kusimidwa pakhomo akangokolola.

“Mavuto ngambiri m’makomo ndiye pomwe munthu sukudziwa n’komwe kuti Admarc idzayamba liti kugula chimanga komanso pamtengo wanji, anthu amangogulitsa kwa mavenda pamtengo uliwonse omwe afuna,” yatero mfumu Khosolo.

Nayo T/A Chadza ya m’boma la Lilongwe yati ndondomekoyi siyidakhale bwino chifukwa ngakhale pulogalamu ikuti kutukula alimi ang’onoang’ono, chimanga chili ndi mavenda kotero ndiwo apindule.

“Adali kuti nthawi yonseyi? Chabwino bola akadalengezeratu anthu atangokolola kuti padzakhala pulogalamu imeneyi koma pano chimanga adagula mavenda moti msikawu ukatsegulidwa, mavenda ndiwo apindule,” yatero mfumu Chadza.

Mfumu yayikulu Maseya ya m’boma la Chikwawa yati idayamba kalekale anthu atangokolola kumene kuwona malonda a chimanga akuchitika mmisika ya Admarc komanso m’misika wamba koma sakudziwa kuti mitengo yake imakhala motani.

“Malonda a chimangawo ndiye adayamba kalekale kuno ndi m’misika ya Admarc yomwe koma sindikukhulupilira kuti mitengo yake idali chonchi, anthu adagulitsa motsika. Koma ena poti kuno timalima chaka chonse mwina apindulako koma apindule kwambiri ndi mavenda,” yatero mfumu Maseya.

Mmodzi mwa alimi, Akim Chaima, wa ku Mitundu m’dera la mfumu Chadza wati iye adali ndi chimanga chankhaninkhani koma adagulitsa kale chifukwa amafuna kubweza ngongole za zipangizo zomwe adatenga.

“Chimanga chambiri ndidagulitsa pamtengo wa K80 pa kilogalamu kwa mavenda miyezi yapitayo kuti ndibweze ngongole. N’kadadziwa kuti kudzakhala msika otere, sin’kadagulitsa ayi,” walira chotero Chaima.

Bungwe la alimi la Farmers’ Union of Malawi (FUM) lati dandaulo la alimiwa ndi lomveka chifukwa ambiri a iwo amalima pogwiritsa ntchito ngongole zomwe amayenera kubwenza pa nthawi yokhazikika.

Mkulu wa FUM Prince Kapondamgaga adati chaka ndi chaka, iwo pamodzi ndi mabungwe ena amalimbikitsa boma kuti lizipereka ndalama mwachangu ku bungwe la Admarc kuti liziyamba kugula chimanga ndi mbewu zina nthawi yabwino.

“Timanena chaka ndi chaka kuti boma limayenera kutsegula misika ya Admarc kumayambiriro, anthu akangokolola kuti mtengo wa boma ndiwo uzilamulira msika. Apa omwe apindule ndi alimi okhawo omwe akadali ndi chimanga koma ambiri angofera fungo,” watero Kapondamgaga.

Iye adati mpofunikaso kuti misika ya Admarc izikhala kufupi ndi alimi kuti asamavutike pankhani ya mayendedwe chifukwa ena amagwa ulesi ndi nkhani ya mayendedwe n’kumagulitsabe kwa mavenda.

Mkulu wa bungwe loimirira mabungwe a zaulimi la Civil Society Agriculture Network (Cisanet), Pamela Kuwali, wati zomwe adandaula alimi ndi mafumu nzoona chifukwa pofika mwezi wa August, alimi ena amakhala atayamba kale kukonzekera ulimi wa chaka chinacho ndiye amafunika zipangizo.

“Nthawiyo ndiye siyidakhaledi bwino chifukwa pano alimi ena adagulitsa kale chimanga chawo pa mtengo wa K70 pa kilogalamu kutanthauza kuti kilogalamu yomweyo akadayipindulira kawiri pa mtengo wa K150,” watero Kuwali.

Mneneri wa Unduna wa malimidwe Osborne Tsoka wavomereza kuti nthawi yotsegulira msika yachedwa koma wati ichi sicholinga cha boma koma zokambirana zina ndi zina ndizo zidachititsa.

“Boma lidapereka kale ndalama zokwana K10 biliyoni zogulira chimanga ndi mbewu zina koma padali zokambirana zokhudza ndondomeko ya kagulidwe zomwe zachedwetsa koma poti zatheka kale, chaka cha mawa tidzatsegula nthawi yabwino,” watero Tsoka.

Iye wati ili ndi phunziro kwa alimi omwe sadekha ndi zokolola zawo monga momwe boma limawalangizira. Iye adati alimi asamapupulume kugulitsa akakolola kuyembekezera kutsegulira kwa Admarc.

M’chikalata cha Admarc, bungwelo lati igula chimanga kwa alimi ang’onoang’ono kudzera m’misika yake pa mtengo wa K150 pa kilogalamu ndipo lati midzi yozungulira msika uliwonse ikuyenera kupanga komiti yoyang’anira momwe malonda aziyendera m’misikayi.

Chikalatacho chati makomitiwo azigwira ntchito ya maso ndi makutu a Admarc podziwitsa bungwelo za zomwe zikuchitika pamsikapo kuti alimi ang’onoang’ono okha ndiwo azigulitsa pa mtengo omwe wakhazikitsidwawu.

Kauniuni wa Tamvani Lolemba ndi Lachiwiri adaonetsa  kuti maboma monga ena Admarc yayamba kale kugula pomwe kwina sanayambe.

Related Articles

Back to top button