Nkhani

Mfumu katunga ibweretsa mpungwepungwe ku Chikwawa

Mfumu Katunga ya m’boma la Chikwawa yabweretsa mpungwepungwe polonga ufumu Gulupu Kaputeni pamene bwalo la milandu la High Court ku Blantyre silinapereke chigamulo pa nkhani yoti oyenelera kuvekedwa ufumuwo ndi yani.

Komanso mfumuyi siyidalabadire zimene Paramount Chief Lundu ya m’deralo idagamula kuti a Kaputeni sakuyenera kugwira ntchito iliyonse ngati gulupu mpaka khoti litapereka chigamulo chake.

Mlanduwo uli kubwalo la High Court

A Kaputeni, omwe dzina lawo ndi Maclean Kaputeni Delemani, akhala ali mfumu yaing’ono Njelera kopitilira zaka 15 ndipo pano akufuna kukhala Gulupu Kaputeni mmalo mwa mayi Chrissy Chizenga amene mbumba ya kubanja idawasankha.

Chodabwitsa n’choti poyamba Mfumu Katunga yomweyo idalamulanso kuti a Maclean Kaputeni sakuyenera kukhala gulupu malinga ndi chiganizo cha banja la ufumuwo limene lidasankha mayi Chizenga.

Izi zitachitika a Kaputeni anaitengera nkhaniyo kubwalo la Mfumu Lundu yemwenso ataunguza nkhaniyi adagamula kuti banja lisankhe munthu wina kuti akhale gulupu osati a Kaputeni chifukwa iwowo ndi mfumu kale Njelera.

Ufumu umenewu umayenda m’mabanja atatu omwe ndi a Mzikiti lomwe ndi bele loyamba, Masavula lomwe ndi banja lachiwiri lomwenso mumachokera a Maclean Kaputeni ndi banja lotsiriza la a M’balirathengo.

A Lundu adalembera a Katunga

Mayi Chizenga amachoka m’banja loyamba la a Mzikiti ndipo ndi mwana wa a Gulupu Kaputeni (Dyna Tsamila) omwe adamwalira m’chaka cha 2019.

Mabanja onse atatuwa adasankha a Chizenga kuti alowe mmalo mwa malemu mayi awo kutengeranso kuti mabanja ena awiriwo muli kale maufumu ena.

Posakhutira ndi zigamulo za a mfumu Katunga ndi Lundu, a Kaputeni adakasuma ku High Court koma chodabwitsa nchoti pamene anthu akudikilira chigamulo cha khoti, Mfumu Katunga yatembenuka ndipo yawaveka a Kaputeni kukhala gulupu. Mwambowu udachitika Loweruka pa December 4 2021.

Malinga ndi kalata zomwe taona kuchokera kwa Lundu komanso zolembedwa ndi oimira a Chizenga pa mlanduwo, zomwe idachita Mfumu Katunga n’zosemphana ndi malamulo.

M’kalata yake imene adalemba pa 1 November 2021, a Lundu adachenjeza a Katunga chifukwa chosalabadira chigamulo chimene bwalo lawo lidapereka kuletsa a Kaputeni kugwira ntchito ngati gulupu.

Adalemba motere a Lundu: “Ndinu nomwe gogo chalo Katunga amene munanditumizira nkhani ya ufumu wa a Kaputeni malingana ndi kusamvetsetsana kwawo pankhaniyi. Bwalo langa litaunikira, tinaona kuti munthu woyenera kukhala pa ufumu wa Kaputeni ndi Chrissy Chizenga yemwe anasankhidwa ndi a mtundu chifukwa cha kumwalira kwa malemu Dyna Tsamira amene ankayendetsa ufumu wa Kaputeni.

“Chifukwa chosakhutitsidwa ndi chigamulo changa a Maclean anakadandaula ku High Court ndiye choncho ndikudabwa kuti inu a T/A Katunga mukugwiritsa ntchito anthu omwe bwalo langa linawapeza osayenera kugwira ntchito ya ufumu. Tinene kuti inu ndi ine wamkulu ndi inuyo.”

Mfumu Lundu inatsindika kuti popeza nkhani ili ku High Court, chigamulo chimene chinaperekedwa ndi bwalo lawo chikhala chomwecho kufikira a High Court adzapereke chigamulo chawo.

Ndipo mu kalata yawo imene analemba pa November 15 2021 atamva kuti Mfumu Katunga inali kalikiliki kukonzekera kuveka a Kaputeni ufumu, oimira a Chizenga pa mlanduwu a Dan Kalaya adaopseza Mfumu Katunga kuti asapitirize kuveka Maclean ngati gulupu chifukwa nkhani idakali m’khoti.

“Zimene mukuchita n’kufuna kusokoneza ndondomeko ya bwalo la milandu pa mlandu umenewu kumenenso kuli kuderera mabwalo a milandu.

“Dziwani kuti ngati mutapitirize ndi maganizo anu ofuna kuveka ufumu a Kaputeni mosemphana ndi chigamulo chimene munapereka nokha komanso chimene anapereka a Paramount Chief Lundu tikapempha kubwalo la milandu kuti m’mangidwe chifukwa chosokoneza ndondomeko za mabwalo a milandu,” anatero a Kalaya.

Koma polankhula ndi Msangulutso Lachinayi, a Katunga adati chimene akudziwa nchoti mlandu umenewu unatha kale n’chifukwa anapitiriza kuveka a Kaputeni ngati gulupu.

A Kaputeni anakasuma ku High Court mchaka cha 2020 ndipo mbali ziwirizi zimayenera kukaonekera kubwalo la mkulu ozenga milandu a Mandala Mambulasa kuti akakambirane za tsogolo la mlanduwo.

Related Articles

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

Check Also
Close
Back to top button